musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wachifumu wa atate wake; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.
2 Mafumu 10:2 - Buku Lopatulika Tsono ikakufikani inu kalata iyi, popeza muli nao ana a mbuye wanu, muli naonso magaleta ndi akavalo, ndi mizinda yalinga, ndi zida, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsono akakufikani inu kalata uyu, popeza muli nao ana a mbuye wanu, muli naonso magaleta ndi akavalo, ndi mudzi walinga, ndi zida, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Inu mukusamalira zidzukulu za mbuyanu Ahabu, ndipo muli nawo magaleta, zida zankhondo ndiponso mizinda yamalinga. Nchifukwa chake tsono mukangolandira kalatayi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Inu mukangolandira kalatayi, popeza ana a mbuye wanu ali ndi inu ndiponso muli ndi magaleta ndi akavalo, mzinda wotetezedwa ndi zida zankhondo, |
musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wachifumu wa atate wake; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.
Ndipo anafika kwa mfumu ya Israele ndi kalata, yakuti, Pakulandira kalata iyi, taonani, ndatumiza Naamani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumchiritse khate lake.