koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.
2 Mafumu 1:4 - Buku Lopatulika Chifukwa chake atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nachoka Eliya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nachoka Eliya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake tsono mau a Chauta oti mukauze mfumu ndi aŵa: ‘Iweyo sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.’ ” Ndipo Eliya adapita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Yehova akuti, ‘Iweyo sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ” Ndipo Eliya ananyamuka. |
koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.
Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.
Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.
Masiku ajawo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Namdzera Yesaya mneneri mwana wa Amozi, nanena naye, Atero Yehova, Siyira banja lako; pakuti udzafa, sudzakhala ndi moyo.
Nanena naye Elisa, Kamuuze, kuti, Sudzachira konse; popeza Yehova wandionetsa kuti adzafa ndithu.
Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.
Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m'dzanja la Afilisti.