Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.
2 Mafumu 1:16 - Buku Lopatulika Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Eliya adauza mfumuyo kuti “Chauta akunena kuti, ‘Pamene udaatuma amithenga kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni, kodi ndiye kuti kuno ku Israele kulibe Mulungu woti nkumpempha nzeru?’ Nchifukwa chake Chauta akuti, ‘Iweyo sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Eliya anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chiyani munatumiza amithenga kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, kukafunsa ngati muti muchire? Kodi mu Israeli mulibe Mulungu woti nʼkukuyankhani funso lanu? Choncho, popeza mwachita izi, simudzadzuka pamene mwagonapo; mudzafa ndithu.’ ” |
Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.
Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.
Masiku ajawo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Namdzera Yesaya mneneri mwana wa Amozi, nanena naye, Atero Yehova, Siyira banja lako; pakuti udzafa, sudzakhala ndi moyo.
Motero Gehazi anatsata Naamani. Ndipo pamene Naamani anaona wina alikumthamangira, anatsika pagaleta kukomana naye, nati, Nkwabwino kodi?
Nanena naye Elisa, Kamuuze, kuti, Sudzachira konse; popeza Yehova wandionetsa kuti adzafa ndithu.
Niti mfumu kwa Hazaele, Tenga chaufulu m'dzanja lako, nukakumane naye munthu wa Mulungu, nukafunsire Yehova mwa iye, ndi kuti, Ndidzachira kodi nthenda iyi?
Chifukwa chake ulankhule nao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Aliyense wa nyumba ya Israele wakuutsa mafano ake mumtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadza kwa mneneri, Ine Yehova ndidzamyankhapo monga mwa mafano ake aunyinji;