Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Mafumu 1:1 - Buku Lopatulika

Ndipo atamwalira Ahabu, Mowabu anapandukana ndi Israele.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo atamwalira Ahabu, Mowabu anapandukana ndi Israele.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Atamwalira mfumu Ahabu, Amowabu adaukira Aisraele.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Atamwalira Ahabu, Mowabu anawukira Israeli.

Onani mutuwo



2 Mafumu 1:1
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo.


Pamenepo Davide anaika maboma mu Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.


Masiku ake Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda, nadziikira mfumu okha.


Motero Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Ndipo Alibina anapanduka nthawi yomweyi.


Anakanthanso Mowabu; ndi Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nazo mphatso.


Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.


Madzi adzayenda natuluka m'zotungira zake, ndi mbeu zake zidzakhala ku madzi ambiri, ndi mfumu yake idzamveka koposa Agagi, ndi ufumu wake udzamveketsa.