M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.
2 Akorinto 9:9 - Buku Lopatulika monga kwalembedwa, Anabalalitsa, anapatsa kwa osauka; chilungamo chake chikhale kunthawi yonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 monga kwalembedwa, Anabalalitsa, anapatsa kwa osauka; chilungamo chake chikhale kunthawi yonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Za munthu wotere paja Malembo akuti, “Wapereka mphatso zake moolowa manja kwa anthu osauka. Chilungamo chake nchamuyaya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Paja analemba kuti, “Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya.” |
M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.
Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.
Pakuti njenjete idzawadya ngati chofunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma chilungamo changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chipulumutso changa kumibadwo yonse.
Ndipo tsopano zitsala zitatu izi: chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.
Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu;