pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.
2 Akorinto 9:12 - Buku Lopatulika Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoonadi ntchito imeneyi yomwe mukuchitira anthu a Mulungu, siingoŵathandiza pa zosoŵa zao, komanso chotsatira chake china nchakuti anthu ochuluka adzathokoza Mulungu kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ntchito imene mukugwirayi siyongothandiza kokha anthu a Mulungu kupeza zosowa, komanso ikuthandiza kuti anthu ambiri ayamike Mulungu. |
pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.
Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu.
anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima;
Koma ndinayesa nkofunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wantchito mnzanga ndi msilikali mnzanga, ndiye mtumwi wanu, ndi wonditumikira pa chosowa changa;
Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?