Ndipo Azariya wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki anamyankha, nati, Chiyambire anthu anabwera nazo zopereka kunyumba ya Yehova, tadya, takhuta, ndipo zitatsalira zambiri; pakuti Yehova anadalitsa anthu ake; ndipo siuku kuchuluka kwa chotsala.
2 Akorinto 9:11 - Buku Lopatulika polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adzakulemeretsani pa zonse, kuti mukhale oolowa manja ndithu, kotero kuti ambiri adzathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yanu imene tiŵatengereko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu. |
Ndipo Azariya wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki anamyankha, nati, Chiyambire anthu anabwera nazo zopereka kunyumba ya Yehova, tadya, takhuta, ndipo zitatsalira zambiri; pakuti Yehova anadalitsa anthu ake; ndipo siuku kuchuluka kwa chotsala.
Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?
kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.
pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.
Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.
ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu;
Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;