Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wake wamkulu: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wake wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkulu wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wake kuti adzakupha iwe.
2 Akorinto 9:1 - Buku Lopatulika Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nkosafunikira kuti ndikulembereni za zopereka zothandizira anthu a Mulungu a ku Yudeya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼkosafunika kuti ndikulembereni za utumiki othandiza anthu a Mulungu. |
Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wake wamkulu: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wake wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkulu wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wake kuti adzakupha iwe.
Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kunena za mau udawamva,
Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.
Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndinena zopeka ine za mfumu, lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.
Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenge kodi chomwe chinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,
Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, chifukwa cha inu; koma kunena za chisankhidwe, ali okondedwa, chifukwa cha makolo.
kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;
Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.
Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.
Ndipo za chija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse.