2 Akorinto 8:22 - Buku Lopatulika Ndipo tinatumiza mbale wathu awaperekeze iwo, amene tamtsimikizira kawirikawiri ali wakhama m'zinthu zambiri, koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukulu kumene ali nako kwa inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tinatumiza mbale wathu awaperekeze iwo, amene tamtsimikizira kawirikawiri ali wakhama m'zinthu zambiri, koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukulu kumene ali nako kwa inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamodzi ndi iwowo tikutuma mbale wathu wina. Takhala tikumuyesa kaŵirikaŵiri, ndipo tampeza kuti ndi wachangu ndithu pa zinthu zambiri. Tsopano akufunitsitsa koposa kuti athandize, popeza kuti amakukhulupirirani kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuwonjezera apo, tikuwatumiza pamodzi ndi mʼbale wathu, amene nthawi zambiri watitsimikizira mʼnjira zosiyanasiyana kuti ndi wachangu ndiponso chifukwa ali ndi chikhulupiriro chachikulu mwa inu. |
Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.