Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m'manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika.
2 Akorinto 8:20 - Buku Lopatulika ndi kupewa ichi kuti wina angatitchule za kuchulukira kumene tikutumikira; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi kupewa ichi kuti wina angatitchule za kuchulukira kumene tikutumikira; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sitikufuna kupatsa anthu chifukwa choti azitinenera zoipa pa mayendetsedwe athu a zopereka zachifundo zochulukazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tikufuna kupewa kutikayikira kulikonse za mmene tikuyendetsera mphatso zochulukazi. |
Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m'manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi makalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.
Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.
ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu;