Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayende naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsate mapazi omwewo kodi?
2 Akorinto 8:17 - Buku Lopatulika Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, anatulukira kunka kwa inu mwini wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, anatulukira kunka kwa inu mwini wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti sadangochita zimene tidampempha, koma changu chake chinali chachikulu, kotero kuti adatsimikiza yekha zobwera kwanuko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Tito sanangovomera kokha pempho lathu, koma yekha anafunitsitsa kwambiri kubwera kwa inu mwa iye yekha. |
Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayende naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsate mapazi omwewo kodi?
Ndipo m'menemo nditchula choyesa ine; pakuti chimene chipindulira inu, amene munayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira.
Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.
Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso.
Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mau a chidandauliro; pakutinso ndalembera inu mwachidule.