Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Akorinto 8:13 - Buku Lopatulika

Pakuti sinditero kuti ena akamasuke, ndi inu musautsidwe;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakuti sinditero kuti ena akamasuke, ndi inu musautsidwe;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Sindikufuna kunena kuti inuyo muvutike, ena apepukidwe, ai, koma kuti pakhale kulingana.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Cholinga chathu sikuti tipeputse ena pamene inuyo mukuvutika, koma kuti pakhale kufanana.

Onani mutuwo



2 Akorinto 8:13
5 Mawu Ofanana  

Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.


Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ake a izo adazigulitsa,


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


koma mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusowa kwao nthawi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwao kukwanire kusowa kwanu.