ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
2 Akorinto 6:14 - Buku Lopatulika Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musamasenze goli pamodzi ndi osakhulupirira. Kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kulungama ndi kusalungama? Kapena kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kuwala ndi mdima? |
ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.
Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.
Ndipo anaimika dzanja lao kuti adzachotsa akazi ao; ndipo popeza adapalamuladi, anapereka nsembe nkhosa yamphongo ya zoweta pa kupalamula kwao.
Za oyera mtima okhala padziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.
ndipo ungatengereko ana ako aamuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao aakazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao.
Muzisunga malemba anga. Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamavala chovala cha nsalu za mitundu iwiri zosokonezana.
Yuda wachita monyenga, ndi mu Israele ndi mu Yerusalemu mwachitika chonyansa; pakuti Yuda waipsa chipatuliko cha Yehova chimene achikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.
Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.
Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.
Ndipo m'mene anamasulidwa, anadza kwa anzao a iwo okha, nawauza zilizonse ansembe aakulu ndi akulu adanena nao.
Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.
Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.
kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,
Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.