2 Akorinto 6:13 - Buku Lopatulika Ndipo kukhale chibwezero chomwechi (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kukhale chibwezero chomwechi (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikulankhula nanu ngati ana anga. Mutibwezere zomwezo zimene ifenso tidakuchitirani inu, pakutitsekulira mtima wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pofuna kufanana zochita ndi kuyankhula monga kwa ana anga, nanunso muzinena za kukhosi kwanu. |
Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza kukuchotsa kudziko la Ejipito; yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.
Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu zilizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.
Abale, ndikupemphani, khalani monga ine, pakuti inenso ndili monga inu. Simunandichitire choipa ine;
Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu aumbika mwa inu,
monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha,
Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama;
Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakuchita cholungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama: