Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli.
2 Akorinto 5:13 - Buku Lopatulika Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati tidachita ngati tapenga, tidachita zimenezi kuti tilemekeze Mulungu. Koma ngati tikuchita zanzeru, tikuchita zanzeru kuti tikuthandizeni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati ndife amisala, monga amanenera ena, nʼchifukwa chofuna kuti Mulungu alemekezedwe. Ngati si ife amisala, nʼkuti inu muthandizike. |
Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli.
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.
Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewere ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.
Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru; pakuti ndidzanena choonadi; koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine.
Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinachita chifukwa cha iye amene anachita choipa, kapena chifukwa cha iye amene anachitidwa choipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.
Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;
kuti Uthenga Wabwino wathu sunadze kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu.
Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.