Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
2 Akorinto 4:17 - Buku Lopatulika Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. |
Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Ha! Kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu, kumene munachitira iwo akukhulupirira Inu, pamaso pa ana a anthu!
Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.
M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa chikhalire ndidzakuchitira chifundo, ati Yehova Mombolo wako.
Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira ntchito iye amene amlindirira Iye.
Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu mu Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.
Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi chimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikulu Kumwamba; pakuti makolo ao anawachitira aneneri zonga zomwezo.
koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'mizinda yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.
kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;
Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.
ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso padzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.
koma monga kulembedwa, Zimene diso silinazione, ndi khutu silinazimve, nisizinalowe mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.
Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.
Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;
kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu mu Mipingo ya Mulungu, chifukwa cha chipiriro chanu, ndi chikhulupiriro chanu, m'mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva;
Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.
Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;
Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.
Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.
Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m'kukondwera,