Ndipo Iye adzaononga m'phiri limeneli chophimba nkhope chovundikira mitundu yonse ya anthu, ndi nsalu yokuta amitundu onse.
2 Akorinto 3:15 - Buku Lopatulika Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pamtima pao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pamtima pao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithu, mpaka lero lino nthaŵi zonse akamaŵerenga Malamulo a Mose, chophimba chija chimaphimbabe mitima yao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale lero lomwe lino akuwerenga mabuku a Mose pali chophimbabe mitima yawo. |
Ndipo Iye adzaononga m'phiri limeneli chophimba nkhope chovundikira mitundu yonse ya anthu, ndi nsalu yokuta amitundu onse.
koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu.