Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa ntchito yanu m'chihema chokomanako.
2 Akorinto 12:13 - Buku Lopatulika Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitse inu? Ndikhululukireni choipa ichi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitsa inu? Ndikhululukireni choipa ichi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi nchiyani chimene ndidachitira mipingo ina, inu osakuchitirani, kupatula chokhachi chakuti sindidakhale ngati katundu wokulemetsani? Ndikhululukireni kulakwa kwangaku. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi inu munaoneka ochepa motani ku mipingo ina, kupatula kuti sindinali cholemetsa kwa inu? Mundikhululukire cholakwa chimenechi! |
Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa ntchito yanu m'chihema chokomanako.
ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yao inali yakusoka mahema.
Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu.
Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana.