Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.
2 Akorinto 12:12 - Buku Lopatulika Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m'chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m'chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidakutsimikizirani mopirira kwambiri kuti ndine mtumwi, pakuchita pakati panu zizindikiro, zozizwitsa ndi ntchito zina zamphamvu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinapirira pokuonetserani zizindikiro za mtumwi weniweni, pochita pakati panu zizindikiro, zodabwitsa ndi ntchito zamphamvu. |
Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.
Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikire, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandire, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandire, mulolana naye bwino lomwe.
Ndipo ndingakhale ndili wosaphunzira m'manenedwe, koma sinditero m'chidziwitso, koma m'zonse tachionetsa kwa inu mwa anthu onse.
koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.