Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m'mizinda yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.
2 Akorinto 11:28 - Buku Lopatulika Popanda zakunjazo pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, chalabadiro cha Mipingo yonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Popanda zakunjazo pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, chalabadiro cha Mipingo yonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimapsinjidwa ndi udindo wa kusamalira mipingo yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa chipsinjo cha nkhawa ya mipingo yonse. |
Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m'mizinda yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.
Atakhala kumeneko nthawi, anachoka, napita ku madera osiyanasiyana a dziko la Galatiya ndi la Frijiya, nakhazikitsa ophunzira onse.
Pamenepo ndipo Mpingo wa mu Yudeya yense ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.
Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndili mtumwi wa anthu amitundu, ndilemekeza utumiki wanga;
kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.
amene anapereka khosi lao chifukwa cha moyo wanga; amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso Mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu;
Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika mu Mipingo yonse.
Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndili nayo chifukwa cha inu, ndi iwowa a mu Laodikea, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;