Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;
2 Akorinto 11:24 - Buku Lopatulika Kwa Ayuda ndinalandira kasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kwa Ayuda ndinalandira kasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kasanu Ayuda adandikwapula mikwapulo 39. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Andikwapulapo kasanu zikoti zija za Ayuda, makumi anayi kuchotsapo chimodzi. |
Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;
Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.
Ndipo kapolo uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sanakonze, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.