Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.
2 Akorinto 11:21 - Buku Lopatulika Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nkuchita zotere. Tsopano ndilankhula ngati wopusa: zimene wina aliyense anganyadire, zomwezo inenso ndingathe kuzinyadira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi. Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso. |
Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.
Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira.
Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.
mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; monga osocheretsa, angakhale ali oona;