2 Akorinto 11:19 - Buku Lopatulika Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mumati ndinu anzeru kwambiri, nchifukwa chake anthu opusa mumangoŵalekerera mokondwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mumalolera kukhala ndi zitsiru mokondwera chifukwa mumati ndinu anzeru! |
Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.
Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.
Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sungathe kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;
Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;