Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.
2 Akorinto 11:18 - Buku Lopatulika Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono popeza kuti ambiri akunyadira zapansipano, inenso ndidzatero. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Popeza ambiri akudzitama monga dziko lapansi limachitira, inenso ndidzitamanso. |
Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.
Pamenepo, pakufuna chimene, kodi ndinachitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?
Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.
Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza kumasomphenya ndi mavumbulutso a Ambuye.
Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewere ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.
Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.
Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;