Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.
2 Akorinto 11:17 - Buku Lopatulika Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimene ndimati ndinena panozi si zimene Ambuye afuna kuti ndinene, koma ndikungonyada, monga momwe amachitira wopusa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kudzinyadira kwangaku, sindikuyankhula monga mmene Ambuye akufunira koma ngati chitsiru. |
Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.
Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.
kuti kapena akandiperekeze a ku Masedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingachititsidwe manyazi m'kulimbika kumene.