Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.
2 Akorinto 11:14 - Buku Lopatulika Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimenezitu si zododometsa ai, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu. |
Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.
Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni Uthenga Wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.
Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.
ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m'kuunika;
amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake;
Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.