Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani? Ndi ichi chimene moyo wake uchifuna achichita.
2 Akorinto 11:12 - Buku Lopatulika Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimene ndikuchita tsopano, ndidzazichitabe, kuti ndisaŵapatse mpata onyenga aja amene akufuna danga loti anyadire, ndi kumanena kuti iwonso akugwira ntchito molingana ndi ife. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ndipitiriza kuchita zomwe ndikuchitazi nʼcholinga chakuti ndisapereke mpata kwa amene akufuna kupezera mwayi woti afanane nafe pa zinthu zimene iwowo amadzitamandira. |
Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani? Ndi ichi chimene moyo wake uchifuna achichita.
Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse?
Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu.
Pamenepo, pakufuna chimene, kodi ndinachitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?
ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitse munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.
Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.
Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;