2 Akorinto 11:11 - Buku Lopatulika Chifukwa ninji? Chifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa ninji? Chifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikutero chifukwa chiyani? Kodi monga sindikukondani? Akudziŵa ndi Mulungu kuti ndimakukondani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chiyani ndikutero? Kodi nʼchifukwa choti sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani! |
Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.
Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;
Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, mu Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu,
Choonadi cha Khristu chili mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali za Akaya.
Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.
Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?
Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.
Sindinena ichi kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.
Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.
Yehova Chauta Mulungu, Yehova Chauta Mulungu, Iye adziwa, ndi Israele adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova,
Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.