2 Akorinto 10:17 - Buku Lopatulika Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja Malembo akuti, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.” |
Kuti ndione chokomacho cha osankhika anu, kuti ndikondwere nacho chikondwerero cha anthu anu, kuti ndidzitamandire pamodzi ndi cholowa chanu.
Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.
chomwecho iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zovuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.
Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.
Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso.
pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;