Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko cha amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.
2 Akorinto 1:16 - Buku Lopatulika ndipo popyola kwanu kupita ku Masedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Masedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo popyola kwanu kupita ku Masedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Masedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndidaakonza ulendo wanga kuti ndidzere kwanu popita ku Masedoniya, ndi kuti ndidzerenso kwanu pochokera ku Masedoniyako. Ndinkafuna kuti potero mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga wopita ku Yudeya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinafuna kuti ndidzakuchezereni pa ulendo wanga wopita ku Makedoniya ndi kudzakuonaninso pochokera ku Makedoniyako kuti inu mudzandithandize pa ulendo wanga wopita ku Yudeya. |
Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko cha amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.
Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,
Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.
chifukwa chake munthu asampeputse. Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale.