Pakuti anaumirira Yehova osapatuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.
1 Yohane 5:3 - Buku Lopatulika Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa, |
Pakuti anaumirira Yehova osapatuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.
ndi kuwachitira chifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi Ine, nasunga malamulo anga.
Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,
Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.
Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chao.
Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.
Chotero chilamulo chili choyera, ndi chilangizo chake nchoyera, ndi cholungama, ndi chabwino.
ndi kuchitira chifundo anthu zikwi, a iwo amene akondana ndi Ine nasunga malamulo anga.
Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.
Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israele, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao, ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo; ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu, ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:
Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo.