Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima; ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.
1 Yohane 3:3 - Buku Lopatulika Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi pa Khristu, amadzisandutsa woyera monga momwe Khristuyo ali woyera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera. |
Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima; ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.
Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.
Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi.
Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.
Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.
chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu mu Mwamba, chimene mudachimva kale m'mau a choonadi cha Uthenga Wabwino,
Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo,
kuti poyesedwa olungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha.
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;
Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse;
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;
mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili padziko lapansi m'chilakolako.
Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.
M'menemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tili ife m'dziko lino lapansi.