1 Yohane 2:6 - Buku Lopatulika iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu akamati amakhala mwa Mulungu, zochita zake zizilingana ndi zimene Yesu ankachita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense amene amati amakhala mwa Mulungu, ayenera kukhala moyo umene Yesu ankakhala. |
Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.
ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake;
Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa Iye; kuti akaonekere Iye tikakhale nako kulimbika mtima, osachita manyazi kwa Iye pa kudza kwake.
Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;
Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.
Yense wakukhala mwa Iye sachimwa; yense wakuchimwa sanamuone Iye, ndipo sanamdziwe Iye.
M'menemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tili ife m'dziko lino lapansi.