1 Yohane 2:3 - Buku Lopatulika Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ife timatsimikiza kuti tikumudziwa ngati tikusunga malamulo ake. |
Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.
Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.
Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.
ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;
Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamgonjetsa woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.
Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka muimfa kulowa m'moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda akhala muimfa.
Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m'choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake,
Yense wakukhala mwa Iye sachimwa; yense wakuchimwa sanamuone Iye, ndipo sanamdziwe Iye.
m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye, ndi Iye mwa ife, chifukwa anatipatsako Mzimu wake.
Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu.
Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.
Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kuchita malamulo ake.
Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.
Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, ndipo chinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.
Pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.
Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.