1 Yohane 1:10 - Buku Lopatulika Tikanena kuti sitidachimwe, timuyesa Iye wonama, ndipo mau ake sakhala mwa ife. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tikanena kuti sitidachimwa, timuyesa Iye wonama, ndipo mau ake sakhala mwa ife. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tikanena kuti sitidachimwe, tikumuyesa wonama Mulungu, ndipo mau ake sali mwa ife. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ife tikanena kuti sitinachimwe, tikumutenga Mulungu kukhala wonama, ndipo Mawu ake sali mwa ife. |
Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndili wabodza, ndi kuyesa mau anga opanda pake?
Koma unati, Ndili wosachimwa ndithu; mkwiyo wake wachoka pa ine. Taona, ndidzakuweruza iwe, chifukwa uti, Sindinachimwe.
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamgonjetsa woipayo.
Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;
Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;
Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirire umboni wa Mulungu anauchita wa Mwana wake.
chifukwa cha choonadi chimene chikhala mwa ife, ndipo chidzakhala ndi ife ku nthawi yosatha: