Ndani wachipanga, nachimaliza icho, kutchula mibadwo chiyambire? Ine Yehova, ndine woyamba, ndi pachimaliziro ndine ndemwe.
1 Yohane 1:1 - Buku Lopatulika Chimene chinaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiona m'maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mau a moyo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chimene chinaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiona m'maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mau a moyo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tikukulemberani za Iye uja amene adaalipo kuyambira pa chiyambi, amene tidamumva ndipo tidamuwona ndi maso athu, amene tidampenya ndithu, ndipo tidamkhudza ndi manja athu: Iyeyo ndiye Mau opatsa moyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tikukulalikirani za Mawu a moyo amene analipo kuyambira pachiyambi, amene tinawamva, amene tinawaona ndi maso athu, amene tinawapenyetsetsa, ndipo tinawakhudza ndi manja athu. |
Ndani wachipanga, nachimaliza icho, kutchula mibadwo chiyambire? Ine Yehova, ndine woyamba, ndi pachimaliziro ndine ndemwe.
Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti Ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, monga muona ndili nazo Ine.
Ndipo iye amene anaona, wachita umboni, ndi umboni wake uli woona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zoona, kuti inunso mukakhulupirire.
Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira.
Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha;
Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.
kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;
tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;
Ndipo ife tapenyera, ndipo tichita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.
ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.
Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smirina lemba: Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo: