Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Timoteyo 3:1 - Buku Lopatulika

Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna ntchito yabwino.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna ntchito yabwino.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu akuti, “Ngati munthu afuna ntchito ya kuyang'anira Mpingo, akukhumba ntchito yaulemu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mawu woona ndi awa: Ngati munthu akufunitsitsa atakhala woyangʼanira, ndiye kuti akufuna ntchito yabwino.

Onani mutuwo



1 Timoteyo 3:1
19 Mawu Ofanana  

Chipatso cha wolungama ndi mtengo wa moyo; ndipo wokola mtima ali wanzeru.


Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.


Pakuti kwalembedwa m'buku la Masalimo, Pogonera pake pakhale bwinja, ndipo pasakhale munthu wogonapo; ndipo uyang'aniro wake autenge wina.


Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.


Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndili mtumwi wa anthu amitundu, ndilemekeza utumiki wanga;


kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;


Paulo ndi Timoteo, akapolo a Yesu Khristu, kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:


Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.


Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa;


Okhulupirika mauwa ndi oyenera kulandiridwa konse.


Okhulupirika mauwa: Pakuti ngati tidamwalira ndi Iye, tidzakhalanso moyo ndi Iye:


Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;


Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a ntchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;


ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;


Pakuti munalikusochera ngati nkhosa; koma tsopano mwabwera kwa Mbusa ndi Woyang'anira wa moyo wanu.


Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira;


Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;