Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;
1 Timoteyo 1:8 - Buku Lopatulika Koma mudziwa kuti lamulo ndi labwino, ngati munthu achita nalo monga mwa lamulo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mudziwa kuti lamulo ndi labwino, ngati munthu achita nalo monga mwa lamulo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tikudziŵa kuti Malamulo ngabwino, malinga nkuŵagwiritsa ntchito moyenera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tikudziwa kuti Malamulo ndi abwino ngati munthu awagwiritsa ntchito bwino. |
Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, ndivomerezana nacho chilamulo kuti chili chabwino.
Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza.
Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo.
Koma ngatinso wina ayesana nao m'makani amasewero, samveka korona ngati sanayesane monga adapangana.