1 Samueli 8:22 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Samuele, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu. Ndipo Samuele anati kwa amuna a Israele, Mupite, munthu yense kumzinda wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Samuele, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu. Ndipo Samuele anati kwa amuna a Israele, Mupite, munthu yense kumudzi wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adauza Samuele kuti, “Umvere zimene akunena, ndipo uŵapatse mfumu.” Choncho Samuele adauza Aisraelewo kuti, “Nonse bwererani kwanu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anamuyankha nati, “Amvere zimene akunena ndipo apatse mfumu.” Ndipo Samueli anati kwa Aisraeli aja, “Bwererani aliyense kwawo.” |
Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.
Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.