1 Samueli 7:15 - Buku Lopatulika ndipo Samuele anaweruza Israele masiku onse a moyo wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo Samuele anaweruza Israele masiku onse a moyo wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Samuele adatsogolera Aisraele moyo wake wonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Samueli anatsogolera Aisraeli moyo wake wonse. |
Ndipo Samuele anauza Aisraele onse, kuti, Onani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu.
Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.
Ndipo Samuele anamwalira; ndi Aisraele onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ake, namuika m'nyumba yake ku Rama. Davide ananyamuka, natsikira ku chipululu cha Parani.
Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m'malo onse amenewa.
Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele mu Mizipa.