Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 6:21 - Buku Lopatulika

Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho adatuma amithenga kwa nzika za ku Kiriyati-Yearimu kukanena kuti, “Afilisti abweza Bokosi lachipangano la Chauta. Bwerani kuno, mudzalitenge, kupita nalo kwanuko.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsono iwo anatumiza a mithenga kwa anthu a ku Kiriati-Yearimu kuti, “Afilisti atibwezera Bokosi la Yehova. Bwerani kuno mudzalitenge, mupite nalo kwanuko.”

Onani mutuwo



1 Samueli 6:21
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nachokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amatchula nalo Dzinalo, Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi.


ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo, chihemacho adachimanga mwa anthu;


Ndipo panalinso munthu amene ananenera m'dzina la Yehova, Uriya mwana wake wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu; ndipo iye ananenera mzinda uwu ndi dziko lino monga mwa mau onse a Yeremiya;


Koma pitani tsopano kumalo anga amene anali mu Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona chimene ndinachitira chifukwa cha zoipa za anthu anga Israele.


chifukwa chake ndidzaichitira nyumba iyi, imene itchedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzachitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinachitira Silo.


Kiriyati-Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yao.


Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba paphiri mpaka chitsime cha madzi cha Nefitowa, natulukira malire kumizinda ya phiri la Efuroni; ndipo analemba malire kunka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.


Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kunka kumwera, kuchokera kuphiri pokhala patsogolo pa Betehoroni, kumwera kwake; ndi matulukiro ake anali ku Kiriyati-Baala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mzinda wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo.


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumizinda yao tsiku lachitatu. Koma mizinda yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.


Nakwera namanga misasa mu Kiriyati-Yearimu, mu Yuda; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo chigono cha Dani, mpaka lero; taona, ali m'tseri mwa Kiriyati-Yearimu.