Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, chifukwa cha kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.
1 Samueli 6:20 - Buku Lopatulika Ndipo a ku Betesemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakutichokera ife? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo a ku Betesemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakutichokera ife? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono anthu a ku Betesemesi adati, “Angathe ndani kuima pamaso pa Chauta, Mulungu woyerayu? Ndipo Bokosi lachipanganoli lidzapita kuti likachoka kuno?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono anthu a ku Beti-Semesi anafunsa, “Ndani angathe kuyima pamaso pa Yehova Mulungu Woyera? Bokosi la Chipanganoli lipita kuti likachoka pano?” |
Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, chifukwa cha kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.
Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine?
Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera; ndipo musamadziipsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa pansi.
Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndikhale Mulungu wanu; chifukwa chake mukhale oyera, popeza Ine ndine woyera.
Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka Iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;
Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.
Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa loyandikira anamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa anagwidwa ndi mantha aakulu. Ndipo Iye analowa m'ngalawa, nabwerera.
Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti nchomwecho, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israele lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lake litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.