Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Myebusi.
1 Samueli 6:14 - Buku Lopatulika Ndipo galetalo linafika m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi, ndi kuima momwemo, pamwala waukulu; ndipo anawaza matabwa a galetalo, nazipereka ng'ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo galetalo linafika m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi, ndi kuima momwemo, pa mwala waukulu; ndipo anawaza matabwa a galetalo, nazipereka ng'ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Galeta lija lidafikira ku munda wa Yoswa ku Betesemesi ndi kuima komweko. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu am'mudzimo adaliŵaza nkhuni galetalo ndipo adapha ng'ombezo nazipereka kwa Chauta ngati nsembe yopsereza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Galeta lija linafika ku munda wa Yoswa ku Beti-Semesi ndipo linayima. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu anawaza nkhuni galetalo, ndipo anapha ngʼombe zija ndi kuzipereka ngati nsembe zopsereza kwa Yehova. |
Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Myebusi.
Arauna nati kwa Davide Mbuye wanga mfumu atenge napereke nsembe chomkomera; siizi ng'ombe za nsembe yopsereza, ndi zipangizo ndi zomangira ng'ombe zikhale nkhuni;
Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.
Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.
Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.
Ndipo kunali m'mawa mwake, anthu analawirira mamawa namangako guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika.
numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yachiwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zake uyese chifanizo walikhacho.
Ndipo, onani, Saulo anachokera kumunda alikutsata ng'ombe; nati Saulo, Choliritsa anthu misozi nchiyani? Ndipo anamuuza mau a anthu a ku Yabesi.
nati, Ndiloleni, ndimuke; chifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mzindamo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndichoke, ndikaone abale anga. Chifukwa cha ichi safika ku gome la mfumu.
Ndipo a ku Betesemesi analikumweta tirigu wao m'chigwamo; natukula maso ao, naona likasalo, nakondwera pakuliona.
ndiponso mbewa zagolide, monga chiwerengo cha midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, mizinda ya malinga, ndi midzi yopanda malinga; kufikira ku mwala waukulu, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi.