Ndipo anachokera ku Betele: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efurata: ndipo Rakele anabala navutidwa.
1 Samueli 4:20 - Buku Lopatulika Ndipo pamene adati amwalire, anthu aakazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankhe, kapena kusamalira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene adati amwalire, anthu akazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankhe, kapena kusamalira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Popeza kuti mkaziyo anali pafupi kufa, akazi omuthandiza adamuuza kuti, “Limba mtima, wabala mwana wamwamuna.” Koma iye sadayankhe ngakhale kusamalako ai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Popeza mkaziyo anali pafupi kumwalira, akazi amene amamuthandiza anati, “Usaope, wabereka mwana wamwamuna” Koma iye sanayankhe kapena kulabadirako. |
Ndipo anachokera ku Betele: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efurata: ndipo Rakele anabala navutidwa.
Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa.
Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wabala mwana, sakumbukiranso kusaukako, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu kudziko lapansi.
Ndipo mpongozi wake, mkazi wa Finehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yake yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wake, ndi mwamuna wake anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kuchira kwake kwamdzera.