Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 31:6 - Buku Lopatulika

Chomwecho adamwalira pamodzi Saulo ndi ana ake atatu, ndi wonyamula zida zake, ndi anthu ake onse, tsiku lomwe lija.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chomwecho adamwalira pamodzi Saulo ndi ana ake atatu, ndi wonyamula zida zake, ndi anthu ake onse, tsiku lomwe lija.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Motero Saulo adafa pamodzi ndi ana ake atatu, kudzanso munthu wonyamula zida zake, kuphatikizapo ankhondo ake ambiri, onsewo tsikulo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Motero Sauli ndi ana ake atatu, wonyamula zida zake pamodzi ndi anthu ake onse anafera limodzi pa tsikulo.

Onani mutuwo



1 Samueli 31:6
14 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali atamwalira Saulo, pamene Davide anabwera atawapha Aamaleke, ndipo Davide atakhala ku Zikilagi masiku awiri;


Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.


Momwemo anafa Saulo, ndi ana ake atatu; ndi nyumba yake yonse idafa pamodzi.


Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.


Ndipo anthu onse anapita ku Giligala; ndi kumeneko analonga Saulo mfumu pamaso pa Yehova mu Giligala; ndi pamenepo anaphera nsembe zoyamika pamaso pa Yehova; ndi pomwepo Saulo ndi anthu onse a Israele anakondwera kwakukulu.


Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atumize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti choipa chanu munachichita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, nchachikulu.


Koma mukaumirirabe kuchita choipa, mudzaonongeka, inu ndi mfumu yanu yomwe.


Nati Davide, Pali Yehova, Yehova adzamkantha iye; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako.


Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m'dzanja la Afilisti.


Ndipo pakuona kuti Saulo anafa, wonyamula zida zake yemwe, anagwera lupanga lake, nafera limodzi ndi iye.


Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya mizinda yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo.