Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 31:5 - Buku Lopatulika

Ndipo pakuona kuti Saulo anafa, wonyamula zida zake yemwe, anagwera lupanga lake, nafera limodzi ndi iye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo pakuona kuti Saulo anafa, wonyamula zida zake yemwe, anagwera lupanga lake, nafera limodzi ndi iye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Wonyamula zida uja ataona kuti Saulo wafa, nayenso adadzigwetsa pa lupanga lake nafera naye limodzi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mnyamata wonyamula zida zake uja ataona kuti Sauli wafa, nayenso anadzigwetsera pa lupanga lake nafa naye limodzi.

Onani mutuwo



1 Samueli 31:5
5 Mawu Ofanana  

Kunali tsono, pakuona Zimiri kuti nkhondo yalowa m'mzinda, anakwera pa nsanja ya nyumba ya mfumu, nadzitenthera ndi moto nyumba ya mfumu, nafa;


Ndipo pamene wonyamula zida zake anaona kuti Saulo wafa, anagwera nayenso lupanga lake, nafa.


Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.


Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera.


Chomwecho adamwalira pamodzi Saulo ndi ana ake atatu, ndi wonyamula zida zake, ndi anthu ake onse, tsiku lomwe lija.