1 Samueli 31:3 - Buku Lopatulika Ndipo nkhondoyo inamkulira Saulo kwambiri, oponya mivi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukulu chifukwa cha oponya miviyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo nkhondoyo inamkulira Saulo kwambiri, oponya mivi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukulu chifukwa cha oponya miviyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nkhondo idampanikiza kwambiri Sauloyo, ndipo anthu amauta adampeza namlasa koopsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nkhondo inakula kwambiri mozungulira Sauli ndipo pamene anthu amauta anamupeza, anamuvulaza kwambiri. |
Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? Undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Saulo ndi Yonatani mwana wake anafanso.
Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda paphiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza.
Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m'khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa;
Ndipo munthu anakoka uta wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israele pakati pa maluma a malaya achitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa galeta wake, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.
Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;