Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndiwo amene anamuika Saulo.
1 Samueli 31:11 - Buku Lopatulika Koma pamene a ku Yabesi-Giliyadi anamva zimene Afilisti anamchitira Saulo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pamene a ku Yabesi-Giliyadi anamva zimene Afilisti anamchitira Saulo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma anthu a ku Yabesi-Giliyadi atamva zimene Afilisti adaamchita Saulo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene anthu a ku Yabesi Giliyadi anamva zimene Afilisti anachitira Sauli, |
Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndiwo amene anamuika Saulo.
Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m'khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa;
Nati iwo, Kodi pali lina la mafuko a Israele losakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa? Ndipo taonani, kuchokera ku Yabesi-Giliyadi sanadze mmodzi kumisasa, kumsonkhano.