Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.
1 Samueli 31:1 - Buku Lopatulika Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Afilisti adamenyananso nkhondo ndi Aisraele, ndipo Aisraelewo adathaŵa Afilisti, ndipo ambiri adakaphedwa ku phiri la Gilibowa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa. |
Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.
Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda paphiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza.
Ndipo Yonatani mwana wa Saulo, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi. Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Saulo ndi Yonatani yochokera ku Yezireele; ndipo mlezi wake adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lake ndiye Mefiboseti.
Ndipo kunali masiku aja, Afilisti anasonkhanitsa pamodzi makamu ao onse kunkhondo, kuti akaponyane ndi Aisraele. Ndipo Akisi ananena ndi Davide, Dziwa kuti zoonadi, udzatuluka nane ndi nkhondo, iwe ndi anthu ako.
Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.
Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m'dzanja la Afilisti.
Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Saulo anasonkhanitsa Aisraele onse, namanga iwo ku Gilibowa.
Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisraele anamanga ku chitsime cha mu Yezireele.