Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m'mzinda wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.
1 Samueli 30:29 - Buku Lopatulika ndi kwa iwo a ku Rakala, ndi kwa iwo a ku m'mizinda ya Ayerameele, ndi kwa iwo a m'mizinda ya Akeni; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi kwa iwo a ku Rakala, ndi kwa iwo a ku m'midzi ya Ayerameele, ndi kwa iwo a m'midzi ya Akeni; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa a ku Rakala, a ku mizinda ya fuko la Ayeramiyele, a ku mizinda ya fuko la Akeni, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Rakala, mizinda ya fuko la Ayerahimeeli, mizinda ya fuko la Akeni, |
Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m'mzinda wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.
Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke.
Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu?
Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni.